Discover millions of ebooks, audiobooks, and so much more with a free trial

Only $11.99/month after trial. Cancel anytime.

Iwo Amene Amaiwala
Iwo Amene Amaiwala
Iwo Amene Amaiwala
Ebook135 pages1 hour

Iwo Amene Amaiwala

Rating: 0 out of 5 stars

()

Read preview

About this ebook

Anthu opanduka samakumbukira zomwe zapangidwa kwa iwo ndipo nthawi zambiri amasankha kuiwala zinthu zina. Yudase sanakumbukire zimene Ambuye anamchitira, ndinso sanakumbukirenso zinthu zimene anaona ndi kumva kwa Yesu. Ichi ndi chifukwa chake adakhala mtundu wa munthu amene tikumudziwa lero ngati ‘Yudase’.
Kuthekera kokumbukira ndi chimodzi mwa zinthu zauzimu chomwe mtumiki atha kukhala nacho. Anthu amene samakumbukira, siwamba kuchita bwino. Iwo amalephera kufika mlingo wina. Bukhu lapaderali, pa mutu wosakambidwa kwambiriwu ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu kwa inu.

LanguageEnglish
Release dateMar 22, 2019
ISBN9781641359740
Iwo Amene Amaiwala
Author

Dag Heward-Mills

Bishop Dag Heward-Mills is a medical doctor by profession and the founder of the United Denominations Originating from the Lighthouse Group of Churches (UD-OLGC). The UD-OLGC comprises over three thousand churches pastored by seasoned ministers, groomed and trained in-house. Bishop Dag Heward-Mills oversees this charismatic group of denominations, which operates in over 90 different countries in Africa, Asia, Europe, the Caribbean, Australia, and North and South America. With a ministry spanning over thirty years, Dag Heward-Mills has authored several books with bestsellers including ‘The Art of Leadership’, ‘Loyalty and Disloyalty’, and ‘The Mega Church’. He is considered to be the largest publishing author in Africa, having had his books translated into over 52 languages with more than 40 million copies in print.

Read more from Dag Heward Mills

Related to Iwo Amene Amaiwala

Related ebooks

Christianity For You

View More

Related articles

Reviews for Iwo Amene Amaiwala

Rating: 0 out of 5 stars
0 ratings

0 ratings0 reviews

What did you think?

Tap to rate

Review must be at least 10 words

    Book preview

    Iwo Amene Amaiwala - Dag Heward-Mills

    Kukhulupirika ndi Kusakhulupirika

    Iwo Amene

    AMAIWALA

    DAG HEWARD-MILLS

    Kupatula ngati kutchulidwa kwina, Malemba onse achokera mu Baibulo la Bukhu Lopatulika La Chichewa 1966

    Umwini © 2019 Dag Heward-Mills

    Mutu Woyambirira: Those who Forget

    Kutsindikiza koyamba 2019 ndi Parchment House

    Dziwani zambiri zokhudza Dag Heward-Mills pa:

    Healing Jesus Campaign

    Lemberani kwa: evangelist@daghewardmills.org

    Webusaiti: www.daghewardmills.org

    Facebook: Dag Heward-Mills

    Twitter: @EvangelistDag

    ISBN: 

    Umwini wonse wasungidwa pansi pa umwini lamulo la umwini lapadziko. chilolezo cholembedwa chikuyenera kutengedwa kuchokera kwa wosindikiza kuti mugwiritse ntchito kapena kutulutsa kachikena gawo lili lonse la bukhu limeli, pokha pokha mawu ochepa mu maganizo ofunikira kwambiri kapena nkhani

    Zamkatimu

    Kusalungama kwa Iwo Amene Amaiwala 1

    Zifukwa Zisanu ndi Chimodzi Za kufunika kwa Kukumbukira 13

    Zoipa zisanu Zimene Zimagwera Anthu Amene Amayiwala 22

    Zolakwika Zisanu ndi Zitatu Zomwe Anthu Amakonda Kuiwala 37

    Mifungulo Isanu ndi Iwiri Yomwe Ikakuthandizeni Kukumbukira 60

    Zinthu Zomwe Anthu Olungama Amakumbukira 73

    Zotsatira Zisanu ndi Ziwiri za Kukumbukira 83

    Anthu Omwe Simukuyenera Kuwaiwala 87

    Zikumbutso Zisanu Zomwe Zimalimbana ndi Kuiwala 96

    Mutu 1

    Kusalungama kwa Iwo Amene Amaiwala

    ... Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala...

    Ahebri 6:10

    1. ANTHU AMENE ALI OIWALA NDI OSALUNGAMA.

    PAKUTI MULUNGU SALI WOSALUNGAMA KUTI ADZAIWALA nchito yanu, ndi cikondico mudacionetsera ku dzina lace, umo mudatumikira oyera mtima ndi ku-watumikirabe.

    Ahebri 6:10

    Anthu ambiri amadziwa za machimo aakulu anayi: kunama, kuba, dama ndi kupha. Ngati mu-tati mufunse anthu mndandanda wa machimo iwo sangathe kunena za tchimo la kuiwala. Koma Mawu a Mulungu ali omveka pa nkhaniyi. Kuiwala ndi kusalungama! Kuiwala, kulephera kuvo-mereza, kulephera kukumbukira ndi machimo pamaso pa Mulungu.

    Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zace, kapena mkwatibwi zobvala zace? koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.

    Yeremiya 2:32

    Ndizosamvetsetseka kuganizira za zina zomwe anthu osalungama amaiwala.

    Lemba lopatulika pa nkhani ya kubwerera mmbuyo limasonyeza momwe mkwatibwi sadzaiwala diresi lake laukwati. Diresi laukwati ndi chinthu chofunikira kwambiri kwa mkwatibwi.

    Akwatibwi ambiri amalongosola za diresi lawo laukwati mwansanga, nthawi yaukwati isanafike. Mu Lemba ili, kupusa koiwala Mulungu kukufaniziridwa ndi kuthekera kosayerekezeka kuti mkwatibwi adzaiwala diresi lake laukwati.

    Anthu amakula ndikuiwala omwe anawasamalira, omwe anawadyetsa komanso omwe amawa-konda. Amayiwala omwe adawabweretsa kwa Khristu, omwe adawaukitsa mwa Ambuye ndi omwe anawaika mu utumiki. Kodi n’zotheka kuti anthu akhoza kuiwala anthu omwe adawathandi-za pa njira yofunikira kwambiri pamoyo wawo? Kodi angatembenuke ndikuukira anthu omwe an-awalera? Yankho ndi Inde! Izi zimachitika nthawi zonse.

    Anthu amaiwala Mulungu pamene apambana. Maiko a ku Ulaya asiya Mulungu chifukwa akhala opambana kwambiri. Koma ndi Mulungu amene anawapatsa zomwe ali nazo. Anthu amakhulupiri-ra kuti kulibe Mulungu akakhala mamiliyoneya. Ndi tchimo lokhumudwitsa kwambiri kuiwala amene anakupatsani zonse! Ndithudi, ndiko kusalungama kumene kuli koyenera chilango choopsa kwambiri.

    2. ANTHU AMENE ALI OIWALA NDIWOSALUNGAMA NDIPO ALIBE CHIKHA-LIDWE CHA MULUNGU.

    PAKUTI MULUNGU SALI WOSALUNGAMA KUTI ADZAIWALA nchito yanu, ndi cikondico mudacionetsera ku dzina lace, umo mudatumikira oyera mtima ndi ku-watumikirabe.

    Ahebri 6:10

    Mulungu samayiwala! Munthu amayiwala koma Mulungu samayiwala! Anthu oiwala alibe chikhalidwe cha Mulungu! Ndi chiwonetsero cha chikhalidwe chakugwa cha anthu oipa ndi anthu osokonezeka kuti aiwale zinthu zomwe siziyenera kuiwalidwa.

    Munthu amene amalamulidwa ndi Mau a Mulungu ndi Mzimu wa Mulungu samayiwala zinthu zina.

    Munthu wachilengedwe sakonda kukumbukira omwe adamuthandiza. Munthu wachilengedwe wosapulumutsidwa sakonda kukumbukira kumene adachokerako. Munthu wachilengwedwe safu-na kuti aliyense adziwe momwe adakhalira.

    Koma ichi sichikhalidwe cha Mulungu. Pamene Yesu adayenda padziko lapansi adatiuza kumene adachokera. Iye anati Iye sakanakhoza kuchita kanthu mwa Iye yekha.

    Iye anati Iye amangoyankhula mawu omwe Atate Ake anamupatsa Iye.

    Izi zikusiyana kwambiri ndi munthu wonyada wa wauchimo. Munthu wonyada ndi woipa sa-mawulula chiyambi chake. Iye amakhulupirira kuti ali wodzipangira yekha ndipo amaganiza kuti iye anabwera powonekera ndi mphamvu yake.

    3. ANTHU AMENE ALI OIWALA NDIWOSALUNGAMA NDIPO ADATEM-BEREREDWA KUTI AZAUMA.

    Ngati gumbwa aphuka popanda cinyontho? Ngati mancedza amera popanda madzi? Akali auwisi, sanawaceka, AUMA, asanaume mathengo onse ena. Momwemo mayendedwe a ONSE OIWALA MULUNGU...

    Yobu 8:11-13

    Anthu oiwala anatembereredwa kuti azauma. Loyipa kwambiri ndi tchimo lakuiwala kuti matem-berero amagwera mmiyoyo ya anthu oiwala. Simukufunika kumva themberero likuneneredwa pa moyo wanu poiwala zinthu zofunikira. Malemba Opatulika adalengeza kale kuti iwo akuiwala Mulungu adzafota. Samalani kuti mukumbukire njira zonse zomwe Ambuye akubweretsani inu ndi zinthu zonse zomwe Iye wakuchitirani.

    4. ANTHU OSALUNGAMA SAMAKHALA TCHELU NDI ZOYIPA ZOMWE ZIMAZA CHIFUKWA CHAKUYIWALA

    Ku mitsinje ya ku Babulo, Kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira, Pokumbukila Ziyoni.

    Pa msondodzi uli m’mwemo Tinapacika mazeze athu.

    Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo, Ndipo akutizunza anafuna tisekere, Ndi kuti, Mutiyimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni. Tidati, Tidzayimba bwanji nyimbo ya Yehova M’dziko lacilendo?

    NDIKAKUIWALANI, YERUSALEMU, DZANJA LAMANJA LANGA LIIWALE LUSO LACE.

    LILIME LANGA LIMAMATIKE KU NSAYA ZANGA, NDIKAPANDA KUKUM-BUKILA INU; Ndikapanda kusankha Yerusalemu Koposa cimwemwe canga copambana.

    Masalmo 137: 1-6

    Muyenera kuyamba kukumbukira kwambiri. Amene analemba bukhu la Masalmo anadziwa kuti zingakhale zovuta kuiwala Yerusalemu. Anadzitemberera yekha ngati sakumbukira kumene anachokera. Umu ndi momwe nkhani ya chikumbutso ilili ya patali. Mwinanso mukhoza kungosi-ya kukhala ndi moyo ngati simukukumbukira zinthu zina zake. Lilime lanu lidzagwirana ndi denga la pakamwa panu ngati simungathe kukumbukira komwe Mulungu anakuukitsani. Dzanja lanu lamanja silingathe kulemba cheke pamene mukuiwala zomwe Mulungu wakuchitirani.

    5. ANTHU OSALUNGAMA AMAYIWALA AKAKHUTA, AKAKHALA NDI NYUMBA NDIPONSO AKALEMERA.

    KUTI, MUTADYA NDI KUKHUTA, NDI KUMANGA NYUMBA ZOKOMA, ndi ku-khalamo; ndipo zitacuruka ng’ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitacurukanso siliva wanu ndi golidi wanu, zitacurukanso zonse muli nazo; mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m’dziko la Aigupto, m’nyumba ya akapolo;

    Deuteronomo 8: 12-14

    Kusalungama kwa kuyiwala kawirikawiri kumakhudza anthu omwe ali odzaza! Anthu omwe amakhala m’nyumba zawo amakonda kumayiwala Mulungu. Iwo omwe awonjezera zonse zomwe ali nazo amaiwalanso Mulungu mwansanga. Muyenera kukhala mtundu wa munthu yemwe ali wolemera ndi wochita bwino koma wokumbukira kumene mudachokera. Ndizomvetsa chisoni kuti ambiri olemera amalankhula zambiri koma amapereka pang’ono. Anthu amalankhula za madalitso omwe Mulungu wa wapatsa koma samalemekeza Mulungu chifukwa cha zomwe wachita.

    6. ANTHU OSALUNGAMA AMENE AMAYIWALA NTHAWI ZAMBIRI AMAKHA-LA ANTHU ODZIKWEZA.

    Kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo; ndipo zitacuruka ng’ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitacurukanso siliva wanu ndi golidi wanu, zitacurukanso zonse muli nazo; MTIMA WANU UNGATUKUMUKE, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m’dziko la Aigupto, m’nyumba ya akapolo; ndipo munganene

    Enjoying the preview?
    Page 1 of 1