Discover millions of ebooks, audiobooks, and so much more with a free trial

Only $11.99/month after trial. Cancel anytime.

Iwo Amene Amakusiya
Iwo Amene Amakusiya
Iwo Amene Amakusiya
Ebook196 pages1 hour

Iwo Amene Amakusiya

Rating: 0 out of 5 stars

()

Read preview

About this ebook

Anthu amene amakusiya atha kukuwonongani. Palibe chimene chingalongosera kumva kwa kukhumudwa, kubalalika ndi nkhawa zimene zimadza pamene anthu akukusiyani. Bukhu ili lalembedwa kukuthandizani inu kulimbana ndi chiwonongeko chomwe chimadza pamene anthu akusiyani. Musanyengedwe. Kusiidwa sikwachilendo kwa inu ndi utumiki wanu. Ambiri ena avutika ndi zomwezo. Satana anali wopanduka woyamba ndipo akulimbikitsa opandukira onse kuyambira pamenepo.
Ndi bukhu limeneri mu manja anu, muzachirimika ndi kulimbana ndi mzimu wa kusakhulupirika umene umadza ndi “iwo amene amakusiyani”.

LanguageEnglish
Release dateMar 22, 2019
ISBN9781641359702
Iwo Amene Amakusiya
Author

Dag Heward-Mills

Bishop Dag Heward-Mills is a medical doctor by profession and the founder of the United Denominations Originating from the Lighthouse Group of Churches (UD-OLGC). The UD-OLGC comprises over three thousand churches pastored by seasoned ministers, groomed and trained in-house. Bishop Dag Heward-Mills oversees this charismatic group of denominations, which operates in over 90 different countries in Africa, Asia, Europe, the Caribbean, Australia, and North and South America. With a ministry spanning over thirty years, Dag Heward-Mills has authored several books with bestsellers including ‘The Art of Leadership’, ‘Loyalty and Disloyalty’, and ‘The Mega Church’. He is considered to be the largest publishing author in Africa, having had his books translated into over 52 languages with more than 40 million copies in print.

Read more from Dag Heward Mills

Related to Iwo Amene Amakusiya

Related ebooks

Christianity For You

View More

Related articles

Reviews for Iwo Amene Amakusiya

Rating: 0 out of 5 stars
0 ratings

0 ratings0 reviews

What did you think?

Tap to rate

Review must be at least 10 words

    Book preview

    Iwo Amene Amakusiya - Dag Heward-Mills

    Kukhulupirika ndi Kusakhulupirika

    Iwo Amene

    AMAKUSIYA

    DAG HEWARD-MILLS

    Parchment House

    Kupatula ngati kutchulidwa kwina, Malemba onse achokera mu Baibulo la Bukhu Lopatulika La Chichewa 1966

    Mutu Woyambirira: Those who Leave You

    Copyright © 2019 Dag Heward-Mills

    Kutsindikiza koyamba 2019 ndi Parchment House

    Dziwani zambiri za Dag Heward Mills pa:

    Healing Jesus Campaign

    Email: evangelist@daghewardmills.org

    Website: www.daghewardmills.org

    Facebook: Dag Heward-Mills

    Twitter: @EvangelistDag

    ISBN : 978-1-64135-863-7

    Umwini wonse wasungidwa pansi pa lamulo lachitsindiziko lachilungamo. Chilolezo cholembera chiyenera kutetezedwa kuchokera kwa wofalitsa kuti agwiritse ntchito kapena kubwerezanso gawo lirilonse la bukhu ili, kupatulapo ndemanga zochepa mu ndemanga zakuya kapena nkhani.

    Zamkatimu

    Mutu 1: Chifukwa Chomwe Mulungu Amalolera Anthu Kukusiyani

    Mutu 2: Ziwanda Zomwe Zimagwira Mwa Anthu Amene Amachoka Mwaupandu

    Mutu 3: Mawu Osayankhulidwa a Iwo Amene Amakusiyani

    Mutu 4: Zoneneza za Iwo Amene Amakusiyani

    Mutu 5: Momwe Iwo Amene Amakusiyani Amakhalira Chitsanzo Choipa

    Mutu 6: Momwe Mbewu za Kusakhazikika Zimafesedwera Ndi Iwo Amene Amakusiyani

    Mutu 7: Mbewu za Kukhazikika

    Mutu 8: Masoka a Iwo Amene Amakusiyani

    Mutu 9: Momwe Mungadziwire Iwo Amene Atadzakusiyeni

    Mutu 10: Momwe Mungamenyanirane ndi Mimbulu

    Mutu 11: Zotsatira Zomwe Amene Amachoka ndi Ana Athu Ayenera Kuyembekezera

    Mutu 12: Mmene Mungapempherere Amene Amapangitsa Mavuto Pamene Akusiyani

    Mutu 1

    Chifukwa Chomwe Mulungu Amalolera Anthu Kukusiyani

    Zifukwa Khumi Ndi Zisanu Zomwe Mulungu Amalolera Anthu Kukusiyani

    Pali zifukwa zambiri zomwe Mulungu amalolera kuti anthu akusiyeni ngakhale kukupweteketsani mtima.

    1. Yehova amatha kulola anthu kuti akusiyeni pofuna kukozanso zolakwika pamaziko a utumiki wanu.

    Poyamba utumiki uli wonse, timadzadzidwa ndi mantha makamaka a kulephera. Mantha a kulephera amapangisa ife kutenga thandizo lililose lomwe lapezeka. Poyesetsa kupeza chithandizo, atumiki ambiri amakhala mbali ya anthu olakwika.

    Abrahamu ndi chitsanzo chabwino pa izi. Mulungu anamuuza kuti azisiyanitse ku banja lake ndikuenda ulendo wawutali komanso wachinsinsi kupita ku dziko lachilendo lolonjezedwa. Mmalo modzisiyanitsa ku banja lake monga Mulungu ananenera, Abrahamu anapita ndi azibale ake ena mmodzi mwa iwo odziwika anali Loti.

    Ndipo Yehova anati kwa Abramu, tuluka iwe dziko lako, ndi KWA ABALE AKO, ndi ku nyumba ya atate wako kunka kudziko limene ndizasonyeza iwe.

    Genezesi 12:1

    Ndipo ankwera abramu kuchoka ku Aigupto, iye ndi mkazi wake, ndi zose anali nazo, ndi LOTI PAMODZI NAYE kunka ku dziko la kumwera.

    Genezesi 13:1

    Mavuto onse omwe Abrahamu anakumana nawo anachokera pa kupezeka kwa Loti pa moyo wake. Onani mavuto omwe Abrahamu anakumana nawo chifukwa cha Loti.

    1. Abrahamu anali ndi mavuto a mikangano ndi chisokonezo chifukwa cha Loti. Abrahamu m’kupita kwa nthawi anazisiyanitsa kwa abale ake chifukwa cha Loti (Genezesi 13:7-8).

    2. Abrahamu anamenya nkhondo yomwe sankayenera kumenya chifukwa cha Loti. Abrahamu analanditsa Loti mmanja mwa mfumu Kedorelaomere (Genezesi 14:1-16)

    3. Abrahamu anapembedzera maka chifukwa cha Loti. Abrahamu anayenera kupulumusa mphwake kuchionongeko cha Sodomu ndi Gomora (Genezesi 18:23-33)

    Izi ndi zomwe ndimazitcha zolakwika pa maziko a utumiki. Ndi cholakwika chomwe munthu umapanga poyamba utumiki, ndipo zimadza kamba ka mantha. Zolakwazi zimapangisa anthu olakwika kukhala kumbali yako ngati goli (chipsinjo) pa zonse zomwe umapanga.

    Nthawi zina anthu amakwatira anthu olakwika akamalowa mu utumiki.Mulungu amatha kuchotsa anthu olakwika omwe mwakwatirana nawo pa dziko lapansi pofuna kukumasulani ku goli (chipsinjo) mu m’khosi mwanu.

    Anthu ena omwe anali mbali ya utumiki wanga poyamba salinso mbali ya zomwe ndimapanga pano. Mwina, Ndinawatenga ena mwa iwo chifukwa ndimaopa kuti sindikwanitsa popanda iwo. Kupezeka kwawo kumandipatsa chilimbikitso choti ndipambana. Mulungu mwa zifundo zake anapangitsa kuti ena mwa iwo andisiye. Ngakhale ena mwa iwo ndimawasowa, ndinazindikira kuti Mulungu anawalola kundisiya chifukwa chinali cholakwitsa poyamba kuwatenga mu maso mphenya omanga mpingo.

    2. Yehova amatha kulola anthu kuti akusiyeni pofuna kuti mudzichepetse

    Ndipo mukumbukile njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendesani m’chipululu zaka izi makumi anai, KUTI AKUCHEPETSENI, kukuyesani kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.

    Deuteronomo 8:2

    Ndi zokumana nazo zakudzichepesa kusiidwa, kutaidwa kapena anthu kusiya kugwira nawe ntchito limodzi. Kuchoka kuli konse kumasiya kuwawasa mkamwa mwanu. Nthawi zose munthu akachoka mwadzidzidzi, amasiya mmbuyo manfuso opanda mayankho. Zosayembekezereka zomwe zimalengedwa ndi anthu zimasiya mavuto ndi kudzichepesa kwenikweni.

    Kutatha kubzala ma tchalitchi kwa zaka zambiri, ndinadalitsidwa pokhala ndi mazana a azibusa, anyamata ndi atsikana okhulupirika. Ndinadalitsikaso kukhala ndi ena mwa abale anga kukhala azibusa mu mpingo.

    Komabe, tsiku lina ena mwa achibale anga anandisiya mu utumiki ndikuyamba kupanga zosemphana ndi zomwe ndimaphunzitsa. Chinali chamanyazi kwa ine momwe achibale anga amalimbana ndi kupandukira komanso kusakhulupirika mu mpingo. Tsopano ndinaenera kumenyana ndi banja langa lomwe. Izi zakhala zikundibwerera kangapo kuti ndakhala ndikukwanitsa kupanga anthu ena ambiri kukhala okhulupirika koma kulephera kutero ku banja langa lomwe.

    Ndipo ndinazindikila kuti Mulungu amafuna ndizichepetse mu njira imeneyi. Iye anafuna kundionesa kuti sikuthekera kapena mphamvu kapena chiphunzitso kapenanso ulamuliro koma chisomo chake chokha. Mwina, muli ndi anthu ena omwe anakusiyani. Lolani Mulungu agwire ntchito yake muuzimu yokuchepetsani ku ntchito yake.

    3. Ambuye amatha kulola anthu akusiyeni chifukwa mwalola kuti mamembala anu akhale osadziwa posawaphunzitsa za kukhulupirika ndi kusakhulupirika

    Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri aku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m’kupulukira kwawo, osadziwa kanthu.

    2 Samueli 15:11

    Satana anadya mwa anthu omwe samadziwa (mbuli). Chinyengo nthawi zose chimachulukira pamene anthu sanaonesedwe poyera chilungamo cha mawu. Absalomu anali yekhayo yemwe anakwanisa kutsogolera azimbambo mazana awiri omwe anali ofooka (ophweka) mmalingalilo. Kufooka mmalingalilo kumeneku timakutchaso kusadziwa (umbuli).

    Mfundo za kukhulupirika ndi kusakhulupirika, utate ndi chikumbukiro sizimakonda kuphuzitsidwa mu mipingo. Ndizosadabwitsa mamembala a mumpingo amakhala nyama zophweka za ziwanda za chinyengo zomwe zimadya pa kusadziwa kwawo. Mwina, mwalola kusadziwa pa maphunziro awa kuyende ndi kufala kwa mpingo. Satana watengerapo mwayi pa kusadziwa ndi kuchititsa chisokonezo pakati panu.

    Eya, mpingo wanu utha kuthala odalitsidwa ndi ma uthenga a kuchitabwino, ukwati ndi machilitso koma palibe mwa maphuzitso awa angateteze mpingo wanu ku ziwanda za kusakhulupirika ndi chinyengo.

    Tsiku lina, mbusa wina anandifusa chifukwa chani ndimaphunzitsa za kukhulupirika ndi kusakhulupirika. Moselewula anaonjezera kuti, khululupirika si chinthu choti mkuphuzitsa. Ndichomwe umangolamula.

    Ndipo anapitiliza nati, Ndimakhalidwe anu abwino, umalamula khulupirika kwa anthu amene akuzungulira.

    Posachedwa patatha izi anakanthidwa ndi chinyengo chowawa kuchokera kwa abwenzi ake omwe. Sanakhulupirire kuti izi zimachitika kwa iye. Atakumana ndi izi, kunyogodola pa mabuku ndi ziphuzitso zanga zinasandulika kukhala zozizwitsa. Iye anakhala mmodzi mwa osirira pa maphuziro a kukhulupirika ndipo anayamba kulimbikitsa mabuku anga yekha. Mkutheka simungaziwe ubwino wa kuphunzitsa pokhapokha mutakumana ndi zotsatira za kusadziwa.

    4. Yehova amatha kulola anthu ena akusiyeni chifukwa munanyoza mtumiki mzanu pamene mpingo wake unagawanikana

    …wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka chilango

    Miyambi 17:5

    Nthawi zambiri, timanyoza anthu akakhala mmavuto. Ngat anzake a Yobu timaoneka odziwa zifukwa zomwe zinthu zoipa zikuchitika kwa anthu. Timayanganila pasi anthu omwe ali mmavuto kumaganiza kuti anachita kubweretsa okha mavutowo. Mtima umenewu umatsekula makomo kwa satana kumiyoyo yanthu ndi ku utumiki.

    Tsiku lina ndinakumana ndi azibusa atatu a mpingo wopambana wabwino. Gulu lawo logonjetsa linapangidwa ndi anthu awiri amphamvu othandizila ndi mbusa wamkulu. Mothandizidwa ndi omuthandizilawo Mbusayo anakwanisa kumanga tchalitchi imodzi yaikulu muzindawo. Zimaonneka kuti aliyese amakhamukila ku mpingo wawo. Mpingo watsopanowu unayamba kunyadila pa zovala ndipo amakhala ndi misonkhano ingapo ndi anthu ena kusefukila ndikukhala panja. Podzazidwa ndi chikondwerero pa zipambano zowo anayamba kuika maganizo awo pa zifukwa zomwe mpingo wina sumakula mu tawunimo.

    Iwo ananena zonyoza mbusa wa mpingowo, Anthu amachoka mu mpingo pokhapokha ngati pali mtsogoleri oyipa. Izi ndi chifukwa cha utsogoleri oyipa kuti anthu achoka ku utumiki wake ndikuzajowina ife.

    Nthawi imeneyo sindinaziwe ndikomwe kuti anthu amachoka ku mpingowo ndikukajowina wawowo. Ndimava koyamba kuti mpingowo unali ndi mtsogoleri oyipa. Kunali kovuta kudziwa chotonzedwa ndi mnyozo akamakamba za mpingowo ndi mtdogoleri oyipayo.

    Eya, Sindimakaikira kuti anthu amachoka mu utumiki chifukwa cha utsogoleri oyipa. Koma muyenera kukhala osamala pa maweruzidwe ndi mfundo zanu.

    Kwa zaka zambiri, atsogoleri atatu amenewa anatenga gawo lina la utumiki wawo. Gawo latsopano lililose limabweresa kusintha pa kugawa mofanana mphamvu. Mugawo latsopanoli othandizira awiri aja anamusiya mbusa wamkulu potumiza zipongwe ndi milandu kwa iye. Chilungamo ndichakuti kunyoza mbusa wina kuja kunawachitikira kwa iwo koma mu njira yoononga kwambiri.

    Nditava za vutoli, choyamba chomwe chinachitika kwa ine ndichomwe amkanena za mpingo wa alongo awo ndi mbusa wawo, Anthu amakusiya pokhapokha ukakhala mtsogoleri oyipa. Kod mbusa wakulu pano anali mtogoleri oyipa? Sikwenikweni. Pali zifukwa zambiri chifukwa chomwe anthu amakuchokerani. Koma onetsetsani kuti musatoze aliyese akakhala mmavuto.

    Mudziko langa, pali mwambi omwe umati: Ukaona mzako akupsa ndevu usamuseke. Musafuse kuti analola bwanji ndevu zake kugwira moto. Inu katungeni madzi ndikuwasunga pambali panu kupangira zanu zikagwira moto. Baibulo linati, …wokondwera ndi tsoka sadapulumuka chilango (Miyambi 17:5)

    5. Yehova amatha kulola anthu ena akusiyeni chifukwa tsogolo lanu silikhudzana nawo

    Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana.Kristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Kristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsiriza iyi.

    ANATULUKA MWA IFE, KOMATU SANALI A IFE ; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife koma kudatero kuti aonekekere kuti sali onse a ife

    1 Yohane 2:18-19

    Si aliyese oitanidwa kukhala mbali ya timu yanu. Ndi malingalilo achibadwidwe, timasankha anthu amene tikuona kuti akuenera kukhala nafe. Koma Mulungu anasankha kale anthu omwe ali mbali ya tsogolo lanu.

    Kwa zaka ndakhala ndikukumana nazo zomalola anthu omwe ndimaona ngati azakhala nane mpaka kale kundichokera. Ndakhalaso ndi chosangalatsa chodabwitsa pokumana ndi alowammalo awo. Moona mtima, sindikanasankha anthu ambiri omwe ndilinawo lero. Koma Mulungu anawaitana kuzathandiza kumenya mu utumiki. Musamavutike anthu akachosedwa kwa inu. Nthawi zina zimakhala mkati mwa tsogolo lako kuti anachosedwa ndi kubweresa anthu olowammalo mwake.

    6. Yehova amatha kulola anthu ena kuti akusiyeni kuti uvetsetse momwe Mulungu amavera ana ake akamusiya

    Ndipo iye anati, Munthu wina anali ndi ana amuna awiri; ndipo wang’onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigailenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye anawagaira za moyo wake. Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wango’onoyo anasonkhanitsa zones napita ulendo wake ku dziko lakutari; ndipo komweko anamwaza chuma

    Enjoying the preview?
    Page 1 of 1