Discover millions of ebooks, audiobooks, and so much more with a free trial

Only $11.99/month after trial. Cancel anytime.

Kubwerera m’mbuyo
Kubwerera m’mbuyo
Kubwerera m’mbuyo
Ebook129 pages1 hour

Kubwerera m’mbuyo

Rating: 0 out of 5 stars

()

Read preview

About this ebook

Ngakhale ndi mutu wachilendo, kubwerera m’mbuyo kumachitirana ndi zopezeka mwa wamba mwa Akhristu. Ambiri amayamba, koma si ambiri amene amapirira. Mu bukhuli, Bishopu Dag Heward Mils akuchenjeza, ndi kuwonetsa zifukwa zomwe Mkhristu aliyense akuyenera kukafikira Kumwamba!

LanguageEnglish
Release dateMar 21, 2019
ISBN9781641359641
Kubwerera m’mbuyo
Author

Dag Heward-Mills

Bishop Dag Heward-Mills is a medical doctor by profession and the founder of the United Denominations Originating from the Lighthouse Group of Churches (UD-OLGC). The UD-OLGC comprises over three thousand churches pastored by seasoned ministers, groomed and trained in-house. Bishop Dag Heward-Mills oversees this charismatic group of denominations, which operates in over 90 different countries in Africa, Asia, Europe, the Caribbean, Australia, and North and South America. With a ministry spanning over thirty years, Dag Heward-Mills has authored several books with bestsellers including ‘The Art of Leadership’, ‘Loyalty and Disloyalty’, and ‘The Mega Church’. He is considered to be the largest publishing author in Africa, having had his books translated into over 52 languages with more than 40 million copies in print.

Read more from Dag Heward Mills

Related to Kubwerera m’mbuyo

Related ebooks

Christianity For You

View More

Related articles

Reviews for Kubwerera m’mbuyo

Rating: 0 out of 5 stars
0 ratings

0 ratings0 reviews

What did you think?

Tap to rate

Review must be at least 10 words

    Book preview

    Kubwerera m’mbuyo - Dag Heward-Mills

    Kubwerera m’mbuyo

    Tukulani Mphamvu Yanu ya

    Kukhazikika

    DAG HEWARD-MILLS

    Kupatula ngati kutchulidwa kwina, Malemba onse achokera mu Baibulo la Bukhu Lopatulika La Chichewa 1966

    Mawu ochokera kwa Mawu Omaliza a Oyera ndi Ochimwa.

    Kugwiritsidwa ntchito ndi chilolezo cha Kregel Publications

    Mutu Woyambirira: Backsliding - Develop your staying power!

    Umwini © 2019 Dag Heward-Mills

    Kutsindikiza koyamba ndi Parchment House 2019

    Dziwani zambiri zokhudza Dag Heward-Mills

    Healing Jesus Crusade

    Lemberani kwa: evangelist@daghewardmills.org

    Website:  www.daghewardmills.org

    Facebook:  Dag Heward-Mills

    Twitter:  @EvangelistDag

    ISBN:  

    978-1-64135-964-1

    Kuperekedwa:

    Kwa mlongo wanga wamkulu, Beatrix Ayache

    Zikomo chifukwa cha chithandizo chanu kwa zaka zambiri.

    Umwini wonse wasungidwa pansi pa umwini lamulo la umwini lapadziko. Chilolezo cholembedwa chikuyenera kutengedwa kuchokera kwa wosindikiza kuti mugwiritse ntchito kapena kutulutsa kachikena gawo lili lonse la bukhu limeli, pokha pokha mawu ochepa mu maganizo ofunikira kwambiri kapena nkhani.

    Zamkatimu

    Mutu 1: Kubwerera M’mbuyo Nkutani?

    Mutu 2: Mafotokozedwe a mu Baibulo a Kubwerera M’mbuyo

    Mutu 3: Zifukwa Zazikulu Zoyambitsa Kubwerera m’buyo

    Mutu 4: Kalingalilidwe Ka Kubwerela M’mbuyo

    Mutu 5: Zizindikiro Za Kubwerera M’buyo

    Mutu 6: Zizindikiro zina...

    Mutu 7: Zizindikiro Zambiri ...

    Mutu 8: Mfundo Yanga Yomaliza

    Mutu 1

    Kubwerera M’mbuyo Nkutani?

    Mulungu anabweretsa Mneneri Yeremiya pa nthawi yomwe Israeli ndi Yuda anali pafupi kutengedwa ukapolo ndi Babiloni. Iye anagwiritsa ntchito Yeremiya kukawaonetsa anthu a Israeli za kubwerera m’mbuyo kwa mitima yawo.

    Yeremiya, Chifukwa Chani Ululira?

    Bukhu la Yeremiya likulongosola zeni zeni za nyengo zoti munthu wabwerera m’mbuyo. Yeremiya naye wodziwika ngati mneneri wolira, anali ndi ulaliki wake kukhudzana ndi mutu wa kubwerera m’mbuyo. Iye nthawi zambiri anali pa nkhondo ndi anthu a Israeli, mosalekeza kuwachenjedza kuti alape ndi kusintha njira zawo zoipa. Mneneri wolira anakhudzidwa ndi mchitidwe wa anthu ake. Iye anakawalimbikitsa mobwereza bwereza, Siyani njira zanu zoipa. Siyani kuchita choipa! Lapani ndipo mubwerere kwa Mulungu.

    Iye anayesera kuwaonetsa mu njira zosiyana siyana zomwe zimatanthauza kubwerera m’mbuyo. Komabe anthu a Israeli ndi Yuda anakana kusintha.

    Zaka zambiri zapitazo ndinaphunzira kudzera mu zokumana nazo kuti kubwerera m’mbuyo kutha kufanizidwa ndi ndi kuyenda pa nsewu wopanda zizindikiro za pamsewu. Mu kuyenda kwathu kwa Chikhristu mulibe zizindikiro zimenezi zokuchenjezani inu kuti mukubwerea m’mbuyo. Palibe chizindikiro chomwe chimanena kuti, GEHENA NDI CHIONONGEKO-MALIPANDE 200 PATSOGOLO. Palibe chizindikiro chimenecho! Kubwerera m’mbuyo kumadza pang’ono pang’ono, kufikira mutapezeka komwe simumayembekezera. Pang’ono pang’ono koma motsimikizika MUKUSENDEERA kumeneko.

    Kubwerera m’mbuyo ndi koona ndipo kutha kusanthulidwa mu mitundu yosiyana siyana monga monga Jeremiya akulongosolera. Mneneri anagwiritsa ntchito zochitakadi m’moyo kulongosola zopezekeratu wamba muuzimu. Ndi zopezekeratu mu dziko la Chikhristu. Baibulo limati,

    Chomwecho omarizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omarizira.

    Mateyu 20:16

    Mu njira ina, ambiri amayamba ndi Khristu koma ambiri amagwa. Baibulo likunenanso kuti,

    … koma iye wakupirira KUFIKIRA CHIMARIZIRO adzapulumutsidwa.

    Mateyu 10:22

    Ambiri amene amadza kwa Khristu, amagwa pakupita kwa nthawi.

    Ngakhale INU Mutha Kubwerera M’mbuyo!

    Anthu ena amanyoza mutuwu nanena, Sindingabwerera m’mbuyo ine. Mchitidwe womwewu ndi womwe ukuonetsa kuti muli pafupi ndi kubwerera m’mbuyo. Baibulo limatichenjedza ku 1 Akorinto 10:12, Whifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chiriri, ayang’anire kuti ANGAGWE.

    Bukhu limeneri lidzakuthandizani inu kuti mukudze mphamvu yanu yakukhalira mu mpikisano wa Chikhristu. Kuchuluka kwa kudziwa kwanu, kupangitsa inu kuti mutetezedwe-ndipo mphamvu yakukhalira muzakhala nayo. Baibulo limati,

    … pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake.

    2 Akorinto 2:11

    Chiphunzitso cha bukhu ili chidzachotsa vuto la mbuli. Kumbukirani kuti onse amene sawerenga sali abwino kuposa omwe sangawerenge. Munjira ina, iwo amene amakana kufuna funa chidziwitso siabwino kuposa amene alibedi kuthekera kotero.

    Mu mutu ukubwerawu, ndikuonetsani njira zosiyana siyana momwe mungaonere kubwerea m’mbuyo.

    Mutu 2

    Mafotokozedwe a mu Baibulo a Kubwerera M’mbuyo

    Kusinthanitsa Akasupe ndi ZITSIME ZONG’ALUKA

    … anandisiya Ine Kasupe wa madzi amoyo, nadziboolerea zitsime, zitsime zong’aluka, zosakhalamo madzi.

    Yeremiya 2:13

    Pamene ndinali wophunzira wa zachipatala, Ndinatumizidwa kuulendo wantchito ku Danfa, mudzi wa ku Ghana, kwa masabata awiri. Nthawi ina ndili ku ntchito, tinapeza mudzi wina womwe unalibe madzi. Chifukwa choti mudzi unalibe madzi, tinakumba dzenje lalikulu lomwe linatulutsa madzi, nthawi zambiri, madzi amenewa anali akuda komanso a bulauni.

    Ankamwa Madzi Akuda a Bulauni!

    Anthu m’mudzi ankasamba, kunyera komanso kukonzeramo. Pa nthawi yomweyo akamwanso ndi kuphikira madzi omwewo. Madzi amenewa mwachidziwikire ankawapatsa matenda osiyana siyana.

    Mu Baibulo, anthu obwerera m’mbuyo akufanizidwa ndi anthu amene ali ndi kupeza kwa madzi oyenda, koma akusinthanitsa ndi akuda onunkha-monga zomwe ndinaziona kumudzi.

    Ndukhulupirira mutha kudabwa chifukwa ungasiire madzi okoma, abwino, opanda tizilombo, nkukhumba madzi omwe ali ndi tizilombo komanso akuda. Pali okhulupirira ena amene akhala ndi moyo wa chiyero ndi umulungu. Koma, akana kuti akhale moyo wauchimo ndinso wolamuliridwa ndi ziwanda.

    Mulungu wakupatsani china m’malp mwa madzi akuda a bulauni. Mulungu akukuuzani kuti mukabwerera m’mbuyo ndiye kuti mukupita ku chinthu choipa chomwe chi tazakupheni. Akukuuzani kuti musachite china chake chopusa ngati kumwa madzi akuda kachikena.

    Kusandulika Mbewu ya Mpesa Yopanda Pake

    … kodi bwanji wandisandukira Ine mbewu yopanda pake, ya mpesa…?

    Yeremiya 2:21

    Kufotokoza kwina kwa Baibulo ka kubwerera m’mbuyo ndi ngati chomera chabwino chomwe chasandulika mpesa wachilendo wa minga.

    Pano, Mulungu akutionetsa za momwe zomera za mulimi zomwe akuyembekezera kholola labwino likusandukira munda wa minga ndi udzu. Inu, wokhulupirira, ndinu munda chomera chokongola cha Ambuye. Chifukwa chani mufuna kuti musandulike kukhala chitsamba chopanda ntchito? Umu ndi momwe Mulungu amakuonerani mukabwerera m’mbuyo.

    Vuto la Mulungu ndi Israeli linali lakuti Mulungu anaikiza chikondi, chisamaliro ndi nthawi yaikulu mu miyoyo yawo. Koma anasanduka anthu osamvera, ouma mtima komanso oipa. Mulola kuti mukhale cholengedwa chopanda pake pamaso pa Mulungu? Yankho likuyenera kukhala lodziwikiratu kuti Ayi!

    Kusandulika Ngalawa Yolusa

    … ndiwe ngamila yothamanga yoyenda m’njira zake.

    Yeremiya 2:23

    Mkhristu wobwerera m’mbuyo amafotokozedwa ngati bgalawa yothamanga m’njira zake. Ngalawayi ndi yolusa komanso yothamanga, imene imayenda ponse ponse.

    Mtima wa munthu wobwerera m’mbuyo ndi wosalesedwa ngati ngalawa yolusa. Siili pachitsogozo cha china chake. Ndiyomasuka komanso yaukali. Ndukumbukira zaka zina m’mbuyomu ndinakayendera Mkhristu wobwerera m’mbuyo ku London.

    Mzangayu Anali Atalusa

    Njira yabwino yomufotokoza munthuyu

    Enjoying the preview?
    Page 1 of 1