Discover millions of ebooks, audiobooks, and so much more with a free trial

Only $11.99/month after trial. Cancel anytime.

Laikos Anthu Wamba ndi Utumiki
Laikos Anthu Wamba ndi Utumiki
Laikos Anthu Wamba ndi Utumiki
Ebook124 pages1 hour

Laikos Anthu Wamba ndi Utumiki

Rating: 0 out of 5 stars

()

Read preview

About this ebook

Mawu a Chigiriki akuti LAIKOS akutanthauza “kupanda luso”. Mbiri yatiphunzitsa kwa nthawi ndi nthawi kuti zinthu zazikulu zakwaniritsidwa kudzera kwa anthu amene “anasowekera luso”. Phunzirani, kudzera mu bukhu lapamwambali lolembedwa ndi Dag Heward-Mills, zomwe zimachitika pamene palibe anthu a wamba kugwira ntchito mu tchalitchi; momwe mungagawanirane zolemetsa ndi anthu wamba ndi momwe tikuyenera kulimbanira kuteteza utumiki wa wamba.

LanguageEnglish
Release dateMar 27, 2019
ISBN9781643290256
Laikos Anthu Wamba ndi Utumiki
Author

Dag Heward-Mills

Bishop Dag Heward-Mills is a medical doctor by profession and the founder of the United Denominations Originating from the Lighthouse Group of Churches (UD-OLGC). The UD-OLGC comprises over three thousand churches pastored by seasoned ministers, groomed and trained in-house. Bishop Dag Heward-Mills oversees this charismatic group of denominations, which operates in over 90 different countries in Africa, Asia, Europe, the Caribbean, Australia, and North and South America. With a ministry spanning over thirty years, Dag Heward-Mills has authored several books with bestsellers including ‘The Art of Leadership’, ‘Loyalty and Disloyalty’, and ‘The Mega Church’. He is considered to be the largest publishing author in Africa, having had his books translated into over 52 languages with more than 40 million copies in print.

Read more from Dag Heward Mills

Related to Laikos Anthu Wamba ndi Utumiki

Related ebooks

Christianity For You

View More

Related articles

Reviews for Laikos Anthu Wamba ndi Utumiki

Rating: 0 out of 5 stars
0 ratings

0 ratings0 reviews

What did you think?

Tap to rate

Review must be at least 10 words

    Book preview

    Laikos Anthu Wamba ndi Utumiki - Dag Heward-Mills

    LAIKOS

    Anthu Wamba ndi Utumiki

    Anthu wamba

    Abusa Wamba

    Odzipereka

    DAG HEWARD-MILLS

    Kupatula ngati kutchulidwa kwina, Malemba onse achokera mu Baibulo la Bukhu Lopatulika La Chichewa 1966

    Umwini © 2019 Dag Heward-Mills

    Kutsindikiza koyamba 2019 ndi Parchment House

    Dziwani zambiri zokhudza Dag Heward-Mills pa:

    Healing Jesus Campaign

    Lemberani kwa: evangelist@daghewardmills.org

    Webusaiti: www.daghewardmills.org

    Facebook: Dag Heward-Mills

    Twitter: @EvangelistDag

    ISBN: 978-1-64329-025-6

    Umwini wonse wasungidwa pansi pa lamulo la umwini lapadziko. chilolezo cholembedwa chikuyenera kutengedwa kuchokera kwa wosindikiza kuti mugwiritse ntchito kapena kutulutsa kachikena gawo lili lonse la bukhu limeli, pokha pokha mawu ochepa mu maganizo ofunikira kwambiri kapena nkhani.

    Zamkatimu

    Mutu 1: LAIKOS: Munthu Wamba

    Mutu 2: Zomwe Zimachitika Ngati Palibe Anthu Wamba ndi Odzipereka

    Mutu 3: Zifukwa Zisanu ndi Ziwiri Zomwe Mulungu Amagwirira Ntchito Kudzera Mwa Anthu Wamba

    Mutu 4: Zinthu Zisanu ndi Ziwiri Muyenera Kudziwa Zokhudza Utumiki wa Wamba

    Mutu 5: Zifukwa Zhomwe Mukuyenera Kukhalira M’busa Wamba

    Mutu 6: Momwe Ndinagwirira Ngati M’busa Wamba

    Mutu 7: Mmene Mungagawirane Kulemedwa ndi Anthu Wamba

    Mutu 8: M’busa Wamba Wabwino

    Mutu 9: Kodi Khalidwe Labwino la M’busa Wamba ndi Lotani?

    Mutu 10: Abusa Wamba a Mitima Iwiri

    Mutu 11: Kumvetsetsa Momwe Utumiki wa Wamba Uliri Muyezo wa Utumiki

    Mutu 12: Kumvetsetsa Momwe Utumiki wa Wamba Uliri Mtundu wa Utumiki Wothandiza

    Mutu 13: Kumvetsetsa Zosowekera mu Utumiki wa Wamba

    Mutu 14: Kumvesetsa Zifukwa Zimene Mulungu Amalolera Utumiki Wa Wamba Kukhalapo

    Mutu 15: Kuzani Maluso Anayi Ofunika a M’busa Wamba

    Mutu 16: Mabvuto a Abusa a Wamba

    Mutu 17: Utumiki Wokhazikitsa Chitsanzo wa Odzipereka

    Mutu 18: Chifukwa Chomwe Tikuyenera Kulimbana Kuteteza Utumiki wa Wamba

    Mutu 1

    LAIKOS: Munthu Wamba

    Mawu oti munthu wamba adachokera ku mawu a chigiliki oti LAIKOS amane amatanthauza kuti munthu wopanda upangiri. Mbri imatiphunzitsa kuti zinthu zazikulu zikhoza kuchitika kudzera mwa anthu opanda upangiriwa. Kuchita machawi ndikuyang’anitsitsa anthu wamba, kudzakulimbikitsani ndipo mudzawagwiritsa ntchito mu utumiki. Kudzera mwa anthu wamba, miyoyo ya anthu idzapulumuka, milaga idzakhazikika, mipingo idzakula ndipo ntchito ya Mulungu idzayenda bwino.

    Awa ndi matanthauzo ochepa a mawu oti munthu wamba:

    1. Munthu wamba ndi munthu wopanda upangiri.

    2. Munthu wamba ndi munthu wabwinobwino.

    3. Munthu wamba ndi munthu wa ponseponse.

    4. Munthu wamba ndi munthu wachizolowezi.

    5. Munthu wamba ndi munthu wokhazikika.

    6. Munthu wamba ndi munthu wa chabe chabe

    7. Munthu wamba ndi munthu watsiku lililonse.

    8. Munthu wamba ndi munthu wapafupipafupi

    9. Munthu wamba si katswiri.

    10. Munthu wamba ndi munthu amene alibe ukadaulo uliwonse.

    11. Munthu wamba ndi munthu amene siwapaderadera.

    12. Munthu wamba ndi munthu amene alibe luso la mtundu uliwonse.

    13. Munthu wamba ndi amene sadaphunzitsidwe.

    14. Munthu wanba ndi amene alibe zomuyenereza kapena mbiri yabwino.

    15. Munthu wamba ndi munthu amene alibe chilolezo

    Zokwaniritsa Zikuluzikulu mu Mpingo pa Dziko Lonse

    1. Anthu wamba adali nsanamira wa zochitika zosintha tchalitchi.

    Kumasulira kwa baibulo ndi Martin Luther muchiyankhu cha munthu wamba zinasintha dziko lonse. M’malo mongokhala muchilatini, Baibulo lidakhala lowerengeka ndi munthu wamba. Pamene anthu wamba adakhla ndi chivumbulutsa cha chidziwitso, iwo adasintha dziko. Kuzindikira kuti chipulumutso chidali chaulere kwa munthu aliyense kudzera mu chisomo cha Mulungu iwo adadzidzimuka ndi kulimbikitsa kukonzanso kwazinthu.

    2. Anthu wamba ndiye adali nsanamira za mpingo waukulu wa Methodisti

    M’zaka zambiri za m’mbuyomu, chipembedzo cha chimethodisti chinali chipembedzo cha chikulu cha chiprotestanti ku Amerika. Chipembedzochi cha yendetsedwa ndi mphamvu za anthu wamba.

    Chikhalidwe cha kale cholalikira mu mipingo ya chimthodisiti chidali choti olalika wa wamba amasankhidwa kutsogolera mpingo ndi kulalikira m’magulu otchedwa dera

    Olalika wamambayu amayenda kapena kukwera pa kavalo, m’dera loyikika kukalalika molinga ndi ndondomeko ndi nthawi yoikidwayo.

    Ngakhale padali kusankha abusa ndi atumiki, kulalikira kudzera mwa anthu wambaku kudapititirabe ndi alaliki a chipemebedzo cha chimethodisiti. Iwowa amasankhidwa ndi mipingo yosisiyanasisyana kudzalalika mmalo mwa mlaliki wina amene wachokapo.

    3. Anthu wamba adali nsanamira za mpingo umodzi waukulu padziko lonse lapansi.

    Imodzi mwa mfundo zikulu zikulu imene mpingo wa Yoido udamangidwapo, ndiyakugwira ntchito kudzera mwa anthu wamba.

    Mpingo waYoido udayambitsi ndi Davide Yonggi Cho ndipo apongozi ake a Choi Ja-shil, onse amene adali abusa Asembulesi, adali ndi mapemphero a dera pa 15 Meyi, 1958 ndi amayi ena anayi kunyumba kwa Choi Ja-shil.

    Umembala wa tchalichi udafika zikwi zisanu mu chaka cha 1977, namabalayi idawiriza mu zaka ziwiri zosatsatizo. Pa 30 Novembala 1981 nambala ya anthu idakwera kukafika pa zikwi 200. Pa nthawi imeneyi, uwu udali mpingo waukulu pa dziko lonse ndipo udadziwika ndi nyuzi pepa ya Los Angeles.

    Mu chaka cha 2007, tchalitchi chinali ndi mamembala okwana 830,000 ndi mikumano isanu ndi ziwiri lamulungu lokha muziyankhulo zokwana khumi chisanu ndi chimodzi.

    4. Anthu wamba ndi msanamira za mgwirizano waukulu Wa mipingo yochokera Ku Nigeria ndi Ku Ghana.

    Tchalichi cha Redeemed chaku Nigeria ndi tchalichi cha Pentekositi chimene likulu lake liri ku Ghana imadziwika ndi kugwiritsa ntchito bwino anthu wamba. Onse mwa matchalitchi amenewa ali ndi mgwirizano waukulu wa mipingo ndipo amagwiritsa ntchito anthu wamba kulalika ndi ubusa.

    Tchalichi cha pentekositi chidayambitsidwa ndi James Mckeon, m’ mishonale wotumizidwa ndi tchalichi cha Apositoli cha Ku Bradford, UK kupita ku Gold Coast.

    Chidakula nkukhala ndi ma membala okwana 1.7 miliyoni. Tchalitchi cha Pentekositi chili ndi mipingo yokwana zikwi khumi ndi zitatu mmaiko okwana makumi asanu ndi awiri pa dziko lonse.

    Mu chaka cha 1952, Pa Josiah Akindayomi adayanbitsa mipingo wa Redeemed ku Nigeria.

    Pansi pa ulamuliro wa woyang’anira wa mipingo yonse, M’busa E.A Adeboye mpingowu wakula kufikira mmaiko oposa zana limodzi ndi makumi anayi ndi ma miliyoni a mamembala.

    Zoonadi uku nkukwaniritsa zazikulu ndithu ndipo izi zidatheka chifukwa chogwiritsa ntchito anthu wamba.

    Zokwaniritsa Zazikulu mu Dziko la Chikunja

    1. Boma la demokalase lidayambidwa ndi anthu wamba

    Demokalase ndikupereka mwayi ofanana kwa anthu kuti achitepo kanthu ndi kusintha boma lawo ngati akufuna.

    Demokalase ndi mphamvu ya anthu wamba kukana kukhala nyengo zimene sakukondwera nazo.

    Demokalase nkutengapo mbali kwa anthu wamba ndikuchitsa zinthu kusintha mu dziko.

    Demokalase idamangidwa pa mfundo yopereka mwayi ofanana kwa anthu wamba.

    2. Dziko lamphamvu yaikulu lidayamba chifukwa cha anthu wamba.

    Kusintha kwa Amerika ndi chitsanzo

    Enjoying the preview?
    Page 1 of 1