Discover millions of ebooks, audiobooks, and so much more with a free trial

Only $11.99/month after trial. Cancel anytime.

Kupeza Kudzoza
Kupeza Kudzoza
Kupeza Kudzoza
Ebook81 pages48 minutes

Kupeza Kudzoza

Rating: 0 out of 5 stars

()

Read preview

About this ebook

Kudzoza ndi chifungulo chachichikulu chofunikira kutsegula khomo la kuchita bwino ndo kukwaniritsa utumiki. Anthu ambiri ayesera kuchita ntchito ya Mulungu chifukwa cha mafuno abwino, popanda kufika kutali analephera kuzindikira kuti “Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu Wanga (Kudzoza)” [Zekariya 4:4].
Bukhu lapderali “Kupeza Kudzoza” lolembedwa ndi Bishopu Dag Heward-mills lizakuphunzitsani inu zomwe zimatanthauza kupeza kudzoza ndi momwe mungapangire! Lolani chikhumbo khumbo cha Kudzoza kwa Mulungu kutakasike mkati mwanu kudzera mu masamba a m’bukhuli!

LanguageEnglish
Release dateMar 21, 2019
ISBN9781641359658
Kupeza Kudzoza
Author

Dag Heward-Mills

Bishop Dag Heward-Mills is a medical doctor by profession and the founder of the United Denominations Originating from the Lighthouse Group of Churches (UD-OLGC). The UD-OLGC comprises over three thousand churches pastored by seasoned ministers, groomed and trained in-house. Bishop Dag Heward-Mills oversees this charismatic group of denominations, which operates in over 90 different countries in Africa, Asia, Europe, the Caribbean, Australia, and North and South America. With a ministry spanning over thirty years, Dag Heward-Mills has authored several books with bestsellers including ‘The Art of Leadership’, ‘Loyalty and Disloyalty’, and ‘The Mega Church’. He is considered to be the largest publishing author in Africa, having had his books translated into over 52 languages with more than 40 million copies in print.

Read more from Dag Heward Mills

Related to Kupeza Kudzoza

Related ebooks

Christianity For You

View More

Related articles

Reviews for Kupeza Kudzoza

Rating: 0 out of 5 stars
0 ratings

0 ratings0 reviews

What did you think?

Tap to rate

Review must be at least 10 words

    Book preview

    Kupeza Kudzoza - Dag Heward-Mills

    Kupeza

    Kudzoza

    DAG HEWARD-MILLS

    Parchment House

    Kupatula ngati kutchulidwa kwina, Malemba onse achokera mu Baibulo la Bukhu Lopatulika La Chichewa 1966

    Mutu Woyambirira: Catch the Anointing

    Mawu otengedwa kuchokera mu A Passion For The Gospel (Chilakolako Cha Uthenga Wabwino) ndi Colin Whittaker. Kugwiritsidwa ntchito ndi chilolezo cha Kingsway Publications, Lathbridge Drove, Eastbourne, BN23 6NT

    Mawu otengedwa kuchokera mu Understanding the Anointing (Kumvetsetsa Kudzoza) ndi Kenneth Hagin. Kugwiritsidwa ntchito ndi chilolezo cha Faith Library Publications & Kenneth Hagin Ministries Inc.

    Mawu otengedwa kuchokera mu All Things are Possible (Zonse ndi Zotheka) ndi David Edwin Harrel Jnr. Kugwiritsidwa ntchito ndi chilolezo cha Indiana University Press

    Mawu otengedwa kuchokera mu The Release of Power (Kumasulidwa kwa Mphamvu) ndi Bishop David A. Oyedepo. Kugwiritsidwa ntchito ndi chilolezo cha Dominion Publishing House

    Mawu otengedwa kuchokera mu Tragedy Trauma Triumph - WHY? (Tsoka Kupyeteka Chipambano-CHIFUKWA?) ndi T.L. Osborne.Kugwiritsidwa ntchito ndi chilolezo cha OSFO International

    Umwini © 2019 Dag Heward-Mills

    Kutsindikiza ndi Parchment House 2019

    Kutsindikiza koyamba ndi Parchment House 2019

    ISBN: 

    Dziwani zambiri zokhudza Dag Heward-Mills pa:

    Healing Jesus Campain

    Lemberani kwa: evangelist@daghewardmills.org

    Webusaiti: www.daghewardmills.org

    Facebook: Dag Heward-Mills

    Twitter: @EvangelistDag

    Kuperekedwa

    Ndikulipereka bukhu ili kwa Bishopu Nicholas Duncan-Williams.

    Zikomo chifukwa chopangira njira mpingo ku Ghana.

    Umwini wonse wasungidwa pansi pa umwini lamulo la umwini lapadziko. chilolezo cholembedwa chikuyenera kutengedwa kuchokera kwa wosindikiza kuti mugwiritse ntchito kapena kutulutsa kachikena gawo lili lonse la bukhu limeli, pokha pokha mawu ochepa mu maganizo ofunikira kwambiri kapena nkhani

    Zamkatimu

    Mutu 1: Muyenera Kukhala Odzozedwa

    Mutu 2: Kulumikizana ndi Anthu a Mulungu

    Mutu 3: Luso la Kumvetsera Matepi

    Mutu 4: Umboni Wanga

    Mutu 5: Pezani Kudzodza

    Mutu 6: Luso la Kulalikira ndi Kudzoza

    Mutu 7: Aman ndi Tsalach

    Mutu 8: Zimphona Zisanu ndi Chimodzi Zimagwira Kudzoza

    Mutu 9: Chifukwa Chimene Anthu Ena Sapezera Kudzoza

    Mutu 1

    Muyenera Kukhala Odzozedwa

    Ndinalibe maphunziro apadera mu utumiki; sindinapite ku sukulu ya Baibulo ndinso kucheza kochepa kwambiri ndi anthu aakulu a Mulungu. Pamene ndinayamba kulowa mu utumiki, ena mwa anthu a Mulungu amene ndinalumikizana nawo, anayamba kukayikira kuitana kwa Mulungu pa moyo wanga. Ndinalibe njira koma ndikugwiritsira ntchito kudzoza komwe kunali pa anthu ena Mulungu akutali kudzera mu matepi ndi mabuku awo.

    Ine ndikukhulupirira kuti ine ndiri wodzozedwa ndi Mzimu Woyera kuti ndiime mu ofesi yanga ya utumiki. Ndili ndi umboni wochuluka wozungulira ine kuti ndikayike za kudzoza pamoyo wanga. Ndikukhulupiliranso kuti chitukuko cha tekinoloje ndi zamakono pa dziko lapansi ndi cholinga chakuthandizira ufumu wa Mulungu ndi utumiki. Tekinoloje yatithandizira kukhala pafupi ndi anthu odzozedwa.

    Ndiko kudzoza kumene mumasowekera

    Pamene Mulungu akutumizirani munthu wa Mulungu, mumapatsidwa mpata wolandira iye ndikugwira kudzoza komwe kuli pa moyo wake. Kudzoza ndi chinthu chachikulu chomwe iwe ndi ine tikufunikira kuchita ntchito ya Mulungu. Mneneri Zakariya ankadziwa kuti chinthu chofunika kwambiri chinali kudzoza. Ndi khamu la ankhondo ai, ndi Mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga (Zekariya 4: 6).

    Elisa anazindikiranso kuti chinthu chimene chinapangitsa utumiki wa Eliya kukhala wopambana chinali kudzoza. Pamene iye anali nawo mwayi, iye anapempha kudzoza. Anthu ena ayenera kuti anapempha ndalama, maphunziro kapena ziyeneretso zomwe Eliya anali nazo. Koma Elisha ankafuna kudzoza!

    Ndipo kunali ataoloka, Eliya adati kwa Elisa, tapempha chimene ndikuchitire, ndisanachotsedwe kwa iwe. Ndipo Elisa anati, mundipatse magawo awiri a mzimu wanu akhale pa ine.

    2 Mafumu 2: 9

    Mu bukhu ili, ndikufuna kugawana nanu za njira yodzoza yomwe siyinenedwa kawirikawiri. Zingamveke zatsopano kwa inu, koma zenizeni. Ngati pali njira iliyonse yomwe mungapezere kudzoza, chonde tengani! Ine sindikupereka ichi monga njira yokha yomwe Mulungu angakudzozereni inu; Ndikugawana nanu zomwe ndalandira kuchokera kwa Ambuye. Ndikugawana nanu zomwe zili m’Baibulo komanso zomveka bwino.

    Anthu ambiri adzalandira kudzoza mwa kumvetsera matepi ndi kuwerenga mabuku, koma samvetsa zomwe zawachitikira. Ambiri mwa iwo omwe adalandira kudzoza kudzera mu njirayi sangathe kuphunzitsa chifukwa sakuwamvetsa bwino. Ndikukhulupirira kuti ndi ntchito yanga kuphunzitsa njira yosavuta komanso yeniyeni yogwirira chofunikira kwambiri pa utumiki - kudzoza.

    Mutu 2

    Kulumikizana ndi Anthu a Mulungu

    Bukhu lina, ndagawana nanu za kufunikira kolumikizana ndi munthu wa Mulungu kuti mudzalandire kudzoza kumene kuli pamoyo wake. N’chifukwa chiyani muyenera kulumikizana ndi

    Enjoying the preview?
    Page 1 of 1