Discover millions of ebooks, audiobooks, and so much more with a free trial

Only $11.99/month after trial. Cancel anytime.

Iwo Amene Ali Ana Oopsa
Iwo Amene Ali Ana Oopsa
Iwo Amene Ali Ana Oopsa
Ebook180 pages1 hour

Iwo Amene Ali Ana Oopsa

Rating: 0 out of 5 stars

()

Read preview

About this ebook

Bukhu iri ndi mphatso ina kuchokera ku cholembera cha Dag Heward-Mills kwa azitumiki onse amene atha kupeza nthawi yowerenga. Bukhuli lizayankha mafunso onse okhuzana ndi momwe mungakwaniritsire kukhala ndi ubale wabwino pakati pa atate ndi ana.
Kudzera mu chiphunzitso cha bukhu limeneri, muzapewa themberero pa moyo wanu ndi kubweretsa kwanokha mdalitso. Atate ndi anthu apadera amene amakuza ana. Popanda atate sipazakhala ana kupitiriza utumiki ku mibadwo ina.
Maitanidwe a Mulungu amakula kapena kufa ndi kuthekera kochitirana ndi atate. Werengani bukhu limeneri ndipo pewani themberero lokhuzana ndi kusalemekeza, kusamvera ndi kukhala ndi ubale woipa ndi atate.

LanguageEnglish
Release dateMar 22, 2019
ISBN9781641359795
Iwo Amene Ali Ana Oopsa
Author

Dag Heward-Mills

Bishop Dag Heward-Mills is a medical doctor by profession and the founder of the United Denominations Originating from the Lighthouse Group of Churches (UD-OLGC). The UD-OLGC comprises over three thousand churches pastored by seasoned ministers, groomed and trained in-house. Bishop Dag Heward-Mills oversees this charismatic group of denominations, which operates in over 90 different countries in Africa, Asia, Europe, the Caribbean, Australia, and North and South America. With a ministry spanning over thirty years, Dag Heward-Mills has authored several books with bestsellers including ‘The Art of Leadership’, ‘Loyalty and Disloyalty’, and ‘The Mega Church’. He is considered to be the largest publishing author in Africa, having had his books translated into over 52 languages with more than 40 million copies in print.

Read more from Dag Heward Mills

Related to Iwo Amene Ali Ana Oopsa

Related ebooks

Christianity For You

View More

Related articles

Reviews for Iwo Amene Ali Ana Oopsa

Rating: 0 out of 5 stars
0 ratings

0 ratings0 reviews

What did you think?

Tap to rate

Review must be at least 10 words

    Book preview

    Iwo Amene Ali Ana Oopsa - Dag Heward-Mills

    Kukhulupirika ndi Kusakhulupirika

    Iwo Amene Ali

    ANA OOPSA

    DAG HEWARD-MILLS

    Ingakhale zinthu zomwe zafotokozedwa mu bukhuli zinachitikadi, tsatanetsatane wina wasinthidwa kuteteza umwini wa anthu popewa kusweka mitima ndi mkwiyo. Kufanana kuli konse ndi munthu komwe kwa fotokozedwa mu bukhuli ndi zongochitika chabe.

    Kupatula ngati kutchulidwa kwina, Malemba onse achokera mu Baibulo la Bukhu Lopatulika La Chichewa 1966

    Mutu Woyambirira: Those who are Dangerous Sons

    Umwini © 2019 Dag Heward-Mills

    Kutsindikiza koyamba 2019 ndi Parchment House

    Dziwani zambiri zokhudza Dag Heward-Mills pa:

    Healing Jesus Campaign

    Lemberani kwa: evangelist@daghewardmills.org

    Webusaiti: www.daghewardmills.org

    Facebook: Dag Heward-Mills

    Twitter: @EvangelistDag

    ISBN : 978-1-64135-979-5

    Umwini wonse wasungidwa pansi pa lamulo la umwini lapadziko. chilolezo cholembedwa chikuyenera kutengedwa kuchokera kwa wosindikiza kuti mugwiritse ntchito kapena kutulutsa kachikena gawo lili lonse la bukhu limeli, pokha pokha mawu ochepa mu maganizo ofunikira kwambiri kapena nkhani

    Zamkatimu

    Mutu 1: Momwe mungazindikirire Tate

    Mutu 2: Momwe Mungadziwire ndi Kulandira Atate Osiyanasiyana pa Nyengo Zosiyana

    Mutu 3: Mitundu Khumi Ya Atate

    Mutu 4: Zifukwa Zisanu ndi Ziwiri Zomwe Mavuto Amafikira kwa Ana Kuchokera kwa Atate

    Mutu 5: Ana Amene Anatenga Mavuto

    Mutu 6: Zizindikiro Zisanu ndi Ziwiri za Mwana Woona

    Mutu 7: Mitundu Inayi Ya Ana

    Mutu 8: Ana Oopsa

    Mutu 10: Mphoto Zitatu za Kulemekeza Atate

    Mutu 11: Mphamvu Zauzimu Zisanu ndi Ziwiri za Atate

    Mutu 12: Momwe Atate Amapingitsira Kukwezedwa komanso Kugwa kwa Ambiri

    Mutu 13: Zizindikiro Zinayi za Tate

    Mutu 14: Zifukwa Makumi Awiri Zomwe Mwana Akuyenera Kukhalira wa Mtundu Wofanana

    Mutu 15: Chifukwa Chiyani Ana Ena Amaona Chovuta Kulemekeza Atate

    Mutu 1

    Momwe mungazindikirire Tate

    Pakuti ngakhale muli nawo nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Kristu, MULIBE ATATE AMBIRI; pakuti mwa Kristu Yesu ine ndinabala Inu mwa Uthenga Wabwino.

    1 Akorinto 4:15

    Mphatso ya tate ndi mphatso yosowa. Si munthu aliyense wa Mulungu ndi tate. Si aliyense amene amaphunzitsa Mawu a Mulungu ndi tate. Si alaliki onse ndi aphunzitsi ozacheza anali atate.

    Si mneneri aliyense ndi tate ndipo Paulo adanena izi kwa Akorinto.

    Tate ndi Mphatso Yosowa

    Padzakhala anthu ambiri omwe angapereke zofunikira pamoyo wanu. Alangizi ndi aphunzitsi amachuluka koma awa ndi wosiyana ndi atate. Choikamo cha tate ndichomvetsetseka. Tate amakupatsani phukusi lathunthu lomwe limapitirira kuposa phunziro abwino. Aphunzitsi amakhudzidwa ndi kupereka phunziro labwino. Mneneri amakhudzidwa ndi kutumikira mphamvu ya Mulungu kupyolera mu masomphenya, maloto ndi mawu achidziwitso. Koma tate amakhudzidwa ndi moyo wanu wonse.

    Chifukwa kubala kumafuna zambiri, palibe atate ambiri! Ndi zophweka kupyola zolembera zokonzedwa kusiyana ndi kupereka chisamaliro chonse. Anthu akhoza kukhala ovuta komanso osayamika kotero kuti tate okha ndi omwe angakhoze kuwayang’anira pa nthawi yaitali.

    Pali abusa ambiri, alaliki ndi aneneri, koma mneneri wobala - ndani angapeze? N’chifukwa chake Paulo anati: Mukhoza kukhala ndi aphunzitsi zikwi khumi koma mulibe atate ambiri.

    Chikhalidwe chofunikira cha tate si msinkhu wake koma kuthekera kobereka pambuyo pa mtundu wake. Mosiyana ndi maganizo ena, pali achinyamata ambiri omwe ali ndi mtima wa utate.

    Mwachirengedwe, anthu nthawi zambiri amakhala atate ali msinkhu wawung’ono. Umboni wa utate uli mwa ana omwe amapangidwa ndi tate. Zimatengera chikondi, kudzipereka komanso kuleza mtima kulera ana. Pamapeto pake, anawo amatsimikizira ku utate wanu.

    Mukayerekezera utumiki wa Eliya ndi Elisha, mwachitsanzo, mudzapeza kusiyana pakati pa mneneri wokhala tate ndi mneneri wosakhala tate. Kusiyana kumeneku kumakhala koyera pamene mukuphunzira mautumiki awo. Poyerekeza mautumiki a Eliya ndi Elisha, mwamsanga mukuwona kusiyana pakati pa mwamuna yemwe ali ndi mtima wa utate ndi yemwe alibe.

    Onse awiri Eliya ndi Elisa anali aneneri abwino kwambiri. Koma Eliya adali ndi mphatso yowonjezera yakukhala tate. Ndicho chifukwa chake iye adali ndi olowa m’malo mwake. Elisa analibe olowa m’malo mwake. Anatemberera Gehazi yemwe anali pafupi naye. Anatemberera Gehazi pamene analakwitsa ndi ndalama. Mtima wa tate sutemberera mwana wake yekhayo.

    Mzimu wobereka ndi chinthu chomwe chimachititsa munthu wa Mulungu kubereka anthu monga iye mwini mu utumiki. Kuyika mwachidule, mphatso yobereka ndichiwonetsero la chikondi cha Mulungu. Zimatengera chikondi kubweretsa anthu omwe sadziwa zomwe zikuchitika kwa iwo.

    Zimatengera chikondi kubweretsa anthu omwe sangakumvetseni kwa zaka zambiri. Zoonadi, Mulungu amatumiza aphunzitsi ambiri, omwe amatumikira miyoyo yathu. Iwo adzatumikira maphunziro ndi mfundo zomwe zimapanga chiphunzitsocho. Koma tate amapita patsogolo masitepi owonjezera. Kuwonjezera pa kukuphunzitsani inu, iye adzatumikira chikondi ndi chipiriro chomwe chikufunikira kukufikitsani inu mu chifuniro changwiro cha Mulungu.

    Zolinga mwa mtumiki zimamupangitsa iye kuyang’ana ungwiro nthawi zonse. Azolinga ndi osafuna kulakwitsa nthawi zambiri siali atate abwino. Nthawi zambiri samayamikira kuti chisomo cha Mulungu chikugwira ntchito pang’onopang’ono pamoyo wa wina. Iwo amaumirira ungwiro nthawi zonse ndipo izo sizingatheke ndi anthu.

    Mutha kulandira munthu wa Mulungu ngati mphunzitsi. Mukhozanso kumulandira monga m’busa. Mungalandire munthu wa Mulungu monga mneneri kapena mlaliki. N’zotheka kumulandira ngati tate.

    Mupeze tate mu moyo uno! Mulandire mphamvu yokonda ndikukhala tate inu eni!

    Mutu 2

    Momwe Mungadziwire ndi Kulandira Atate Osiyanasiyana pa Nyengo Zosiyana

    Mulungu adzakutumizirani atate osiyana mu nthawi zosiyanasiyana.

    Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Kristu, mulibe atate AMBIRI; pakuti mwa Kristu Yesu ine ndinabala Inu mwa Uthenga Wabwino.

    1 Akorinto 4:15

    Mulungu adzatumiza anthu osiyanasiyana kuzakuberekani inu. Woyamba mwa awa ndi tate wanu wapadziko amene muyenera kulandira bwino. Musati muwone tate wanu wapadziko lapansi ngati wa masiku akale yemwe sagwirizana ndi zenizeni za moyo wamakono. Kuwona tate wanu okubalani ngati osayenerera kukulepheretsani inu kuti mulandire nzeru zawo zazikulu.

    Tate wokubalani adzakhala ndi zolephera zake pomubereka. Posakhalitsa kulandirana kuyenera kuyamba ndipo munthu wotsatira amene atumizidwa ndi Ambuye kuzakuberekani inu adzafika powonekera. Kupyolera mu utumiki wake, mudzalandira chisamaliro cha utate kuti muyenera kudutsa mu gawo lotsatira la moyo wanu. Kenaka munthu wina angathe kudzuka amene angadzakhale ndi udindo wa utate m’moyo wanu. Kulandirana kwa mitundu kulikuyenda! Chovala cha utate chapatsidwa kuchokera kwa munthu mmodzi kupita kumzake.

    Pali zinthu zambiri zomwe tate wanu wokubalani samakuyankhulani. Mwinamwake iwo ayenera kulankhula za chirichonse, koma iwo samatero. Kwa ambiri a ife, makolo athu sanatipatse uphungu sitepi ndi sitepi pothandizira kusankha mkazi kapena mwamuna. Makolo otibala ambiri amapereka ndemanga pa zinthu zosiyanasiyana mu banja.

    Izi nthawi zambiri zimakhala zokhudzana ndi uphungu wawo. Tithokoze Mulungu chifukwa cha abusa omwe nthawi zambiri amagwira ntchitoyi ndikutsogolera ana kulowa m’banja. Abusa nthawi zambiri amakhala atate akutsatira mu kulandiranaku.

    Tsiku lina, mwana wanga wamkazi anandifunsa funso lakuti, Adadi, amatha bwanji anthu kutenga mimba?

    Ndinadabwa ndi funso koma ndinayankha kuti, Mulungu amawapanga mimba.

    Koma iye anaumirira kuti, Ndidziwa kuti Mulungu amawapanga mimba koma zimachitika bwanji?

    Ndinanong’ona yankho ndikukwanitsa kusintha mutuwo.

    Kenaka mkazi wanga anandiuza kuti, Uyenera kulankhula ndi ana ako za kugonana.

    Ndinayankha, Chifukwa chiyani ineyo nditero? Iwe ukayankhulane nawo za izo.

    Tinayamba kukangana ndipo anati, Ndiwe mutu wa nyumba kotero kuti ndiwe amene uyenera kulankhula nawo.

    Koma ndinayankha kuti, Ndiwe amayi awo ndipo nthawi zonse mumalankhula nawo, bwanji osalankhulanso nawo za izi?

    Iye anapitiriza, Ndi udindo wako ndipo uyenera kuchita nawo ntchito!

    Koma sindinagwirizane. Ndinagwiritsa ntchito ulamuliro wanga monga mutu wa nyumba ndikumupatsa ntchito yolankhula ndi ana za zinthu zonsezi.

    Mukuona, tinali titafika pamalo pomwe utate athu komanso umake umatha. Tinkafuna kuti Mulungu atumize ena kutumikira ana athu monga tidatumikira ana a anthu ena. Tinali kupemphera kuti tate otsatirawa nkulandira adzawonekere ndikuwathandiza kuwatsogolera ku chitetezo.

    Pakati pa aphunzitsi ndi aphunzitsi mazana ambiri, nthawi zonse ndi kofunika kuzindikira kuti atate ndi ndani. Atate ali ndi kukhudzidwa kwakukulu pa moyo wanu. Zochita zawo zimapitirira kuposa zomwe akunena. Mudzapeza kuti utumiki wawo umakusamalirani mwathunthu. Utumiki wawo uli ndi zotsatira zosasamala zazikulu pa moyo wanu.

    Imodzi mwa zifungulo zozindikirira tate ndi kuzindikira chikondi, chisamaliro ndi malangizo a Atate wathu Wakumwamba chikufalitsidwa kudzera mwa iye kumoyo wanu.

    Anthu ambiri molakwika amaganiza kuti ndimeyi ikunena kuti muli ndi aphunzitsi zikwi khumi koma muli ndi tate mmodzi. Lemba limanena kuti mulibe atate ambiri. Ilo limanena mwa kuyankhula kwina kuti muli ndi atate angapo.

    Yesu anati, Musatchule aliyense atate.

    Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba.

    Mateyu 23: 9

    Izi zili choncho chifukwa palibe munthu amene angathe kukhala tate weniweni. Amuna onse amalephera kugwira ntchitoyi ndipo Atate wa Kumwamba yekha amapereka chitsanzo chomwe tate ali.

    Kodi simunazindikire mmene atate a padziko lapansi amapikisana bwanji ndi ana awo? Ngakhale atate otibala akhoza kuwapweteka kwambiri ndi kuvutitsa kwa ana awo.

    Anthu ambiri amadana ndi atate awo. Ndipo alipo ambiri amene miyoyo yawo imasokonezedwa chifukwa cha atate awo. Uwu ndi umboni wochuluka wakuti kubereka ndi munthu wachibadwidwe wodzala ndi kupanda ungwiro.

    Ichi ndicho chifukwa chake pali kofunika kwa zomwe ndikuzitcha, kulandirana kwa atate.

    Kulandirana kumakhudza Mulungu kutumiza munthu mmodzi ndi mzake kwa magawo osiyanasiyana a moyo wanu ndi utumiki wanu. Ndikofunika kuzindikira anthu osiyanasiyana pamene akuyenda mu moyo wanu.

    Ichi ndi chimene Yesu anali kufotokoza ndi fanizoli mu Mateyu 21. Ndithudi ife tidzaweruzidwa ndi momwe timalandira atate osiyanasiyana omwe Mulungu amatitumizira ife.

    Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa

    Enjoying the preview?
    Page 1 of 1