Discover millions of ebooks, audiobooks, and so much more with a free trial

Only $11.99/month after trial. Cancel anytime.

Zoopsa Zauzimu
Zoopsa Zauzimu
Zoopsa Zauzimu
Ebook113 pages1 hour

Zoopsa Zauzimu

Rating: 0 out of 5 stars

()

Read preview

About this ebook

Mkhristu amayenda mkati kati mwa zoopsa zambiri ndi misampha. Bukhuli likatsekula maso anu ku zoopsa zambiri zobisika zomwe zikudikira kukupwetekani, kuvulaza komanso kuononga. Dzithandizeni nokha, dzipulumutseni nokha kudzera mu bukhu lamphamvu ili la zoopsa zauzimu!

LanguageEnglish
Release dateMar 21, 2019
ISBN9781641359665
Zoopsa Zauzimu
Author

Dag Heward-Mills

Bishop Dag Heward-Mills is a medical doctor by profession and the founder of the United Denominations Originating from the Lighthouse Group of Churches (UD-OLGC). The UD-OLGC comprises over three thousand churches pastored by seasoned ministers, groomed and trained in-house. Bishop Dag Heward-Mills oversees this charismatic group of denominations, which operates in over 90 different countries in Africa, Asia, Europe, the Caribbean, Australia, and North and South America. With a ministry spanning over thirty years, Dag Heward-Mills has authored several books with bestsellers including ‘The Art of Leadership’, ‘Loyalty and Disloyalty’, and ‘The Mega Church’. He is considered to be the largest publishing author in Africa, having had his books translated into over 52 languages with more than 40 million copies in print.

Read more from Dag Heward Mills

Related to Zoopsa Zauzimu

Related ebooks

Christianity For You

View More

Related articles

Reviews for Zoopsa Zauzimu

Rating: 0 out of 5 stars
0 ratings

0 ratings0 reviews

What did you think?

Tap to rate

Review must be at least 10 words

    Book preview

    Zoopsa Zauzimu - Dag Heward-Mills

    Zoopsa Zauzimu

    DAG HEWARD-MILLS

    Kupatula ngati kutchulidwa kwina, Malemba onse achokera mu Baibulo la Bukhu Lopatulika La Chichewa 1966

    Mutu Woyambirira: Spiritual Dangers

    Umwini © 2019 Dag Heward-Mills

    Kutsindikiza koyamba 2019 ndi Parchment House

    Dziwani zambiri zokhudza Dag Heward-Mills pa:

    Healing Jesus Campaign

    Lemberani kwa: evangelist@daghewardmills.org

    Webusaiti: www.daghewardmills.org

    Facebook: Dag Heward-Mills

    Twitter: @EvangelistDag

    ISBN: 978-1-64135-966-5

    Umwini wonse wasungidwa pansi pa lamulo la umwini lapadziko. chilolezo cholembedwa chikuyenera kutengedwa kuchokera kwa wosindikiza kuti mugwiritse ntchito kapena kutulutsa kachikena gawo lili lonse la bukhu limeli, pokha pokha mawu ochepa mu maganizo ofunikira kwambiri kapena nkhani

    Zamkatimu

    Mutu 1: Chifukwa Chani Zinthu Zina Ziyenera Kuchitidwa Moyambirila

    Mutu 2: Chifukwa Chomwe Ufumu wa Mulungu Ukuyenera Kukhalira Chokonda Chanu Choyamba

    Mutu 3: Kuopsa kwa Dama

    Mutu 4: Ndondomeko Zopewera Dama

    Mutu 5: Zifungulo za Uzimu Zopewera Dama

    Mutu 6: Kodi Mkazi Wachiwerewere Ndi Ndani?

    Mutu 7: Zizindikiro za Mkazi Wachiwerewere

    Mutu 8: Mkazi wachiwerewere mu Baibulo

    Mutu 9: Zifunguro Khumi Zotithandiza Kumvetsetsa Zikhumbokhumbo Athu pa Akazi

    Mutu 10: Kuopsya Kokhala Moyo wa Pawiri

    Mutu 11: Mitundu Khumi ya moyo wapawiri

    Mutu 1

    Chifukwa Chani Zinthu Zina Ziyenera Kuchitidwa Moyambirila

    Zisankho za zinthu zolakwikwa ndi zinthu zoopsa kwa Akhristu. Ukakhala munthu wochimwa, umangosankha pakati pa zinthu ziwiwri: zabwino ndi zoipa. Pamene ukukula mwa Ambuye, zisankho zanu zimakhala zochuluka, ndipo mumakhala ndi zambiri zakuti musankhepo.

    Nthawi imeneyi zisankho zanu sizimakhalanso za pakati pa zoipa ndi zabwino koma pakati pa zabwino ndi zabwino. Kutengera pa zimene mukufuna kukachita, pamakhala kawiri kawiri zinthu zochuluka zabwino zakuti mukasankhepo. Pamene mwafika pa malo amenewo kumakhala kofunikila kuti mukazindikile mfundo iyi ya dongosolo la zisankho: Ndi chiti chimene ndichite moyambirila? Yesu adatipatsa vumbulutso lalikulu pa zinthu zina zomwe zikuyenera kuchitidwa zina zisanachitidwe.

    Ndizosangalatsa kukasanthula kuchuluka kwake kwa zinthu zimene Yesu adanena kuti zikuyenera kukachitidwa moyambirila. Pena paliponse pamene Yesu ankalankhula za zinthu zoyambilila kwambiri, adagwiritsa ntchito liwu la chi Greek lakuti proton. Mu bukhu limeneli tikuyang’na pa zinthu za proton; zinthu zomwe Yesu adanena zichitidwe moyambirila.

    Monga M’khristu, mukuyenera kukchita zinthu zoyambirila moyambirila. Zinthu zoyambirila moyambirila zikutanthawuza kuti moyambirila mu nthawi, mndandanda, nambala,sitepe komanso kufunikila.

    Mkhristu akuyenera kukachita zinthu zofunikila kwambiri moyambirila.

    Chifukwa Chani Zinthu Zina Zikuyenera Kukachitidwa Moyambirila?

    1. Chilichonse chimene sichidachitidwe moyambirila chimawonetsa kutsika kufunikila kwake.

    Mulungu amadekha nafe. Ambiri sadamumvere Iye ndipo awonetsa kuti adangopitilila popanda vuto lili lonse. Kufunikila kwa Mawu a Mulungu kukuwonetsa ngati kukusiika pomwe tikupitililabe kuyenda m’kusamvera. Posakhalitsa icho chimene chimawoneka chofunikila kwambiri kuposa chili chonse chimasanduka chosafunikila ndi chosayenerela.

    Lero, ndimatumikira pansi pa kudzoza ndipo ambiri amandilemekeza chifukwa cha utumiki. Koma ngati sindinamvere Mulungu pomwe ndinapanga, ndikanangokhala ngati dotolo chabe. Mkambilano wokhudzana ndi maitanidwe a Mulungu ukanaoneka ngati wosafunikira komanso wosayenera.

    Kukhala pakati pa anzanga a zachipatala m’zipatala zosiyana siyana, lingaliro lakudzakhala m’busa likadakhala lonyozeka. Ndikadatha kunena kwa anzangawo, Tamverani ndikuuzeni lingaliro lopanda nzeru lomwe ndidali nalo. Kodi mukudziwa kuti ndinkafuna kudzakhala m’busa? Pamene ifeyo tidali achinyamata, tidali auzimu kwambiri komanso osatha kukhudzika.

    Kodi mudayamba mutakunanapo ndi anthu achikulire omwe amanena kuti poyambilila adali pa mndandanda wa kukakhala ansembe? Mu ukalamba wawo, amayesera kukabwezeretsapo pa kusamvera kwawo kudzela mwa ana awo.

    Ndikudziwa za munthu amene ankakakamiza mwana wake kukakhala wansembe.

    Adanena kwa mwana wake wamwamuna, Mulungu adandiyitana kuti ndikakhale wansembe koma sindidachite motero. Iweyo ukhale wansembe ndipo ine ndidzakupatsa ndalama komasno katundu aliyense ndipo sudzasowa kanthu. Kumapeto kwa moyo wawo amafuna atabwezeretsa pa umoyo wawo womwe adakhala wakusamvera ndi kusadziphatikiza kuchifuniro cha Mulungu.

    Mzanga wokondedwa, nditha kukutsimikizila kuti pamene ukuchulukitsa mkayendedwe ka njira zako, malamulonso a Mulungu adzawoneka ngati akutali ndi wosafunikila. Chilipo chifukwa chake cha proton.

    Proton, kapenanso kuti, kuchita zinthu zoyambirila moyambirila, amakupulumutsani inu ku chinyengo cha satana. Mulungu adzakusamalani ndipo adzakhala ndi inu pamene mukuyenda m’chifuniro chake.

    2. China chili chonse chimene sichinachitidwe moyambirila chitha kusachitidwa

    Kuchedwa nthawi zambiri kumatanthawuza kuchotsapo chinthucho. China chili chonse chomwe sichidachitidwe moyambilira chitha kusachitidwa. Sindinkadziwa kuti kuchedwetsa china chake kukhonza kudzetsa kuchotserapo chinthucho pa mndandanda wochita.

    Padali tsiku limene ndidayenera kupanga ulendo kuchoka ku London kunka ku New York kukatumikila. Adandiyika pa mndandanda wokatumikila ku Maryland usiku umenewo. Mwatsoka, ndidali ndi manyamukidwe olawilila kwambiri a ndege kuchokera ku bwalo la ndege la Heathrow ku London, kunka ku Amsterdam ndiye kenako ndimayenera kukalumikiza kuchoka ku Amsterdam kuja kupita ku New York. Mwa mtundu wina wake sindidakhulupilire za nthawi yomwe ndidawona ya chiphaso changa cha ndege. Ndinkalingalira kuti nthawiyo idali yolawirila kwambiri kusiyana ndi m’mene imayenela kukhalila yolondola.

    Pomwe ndidafika ku bwalo la ndegelo, kwa nthawi yoyamba m’moyo wanga, ndidali nditachedwa kwambiri kuti ndithe kukwera nawo ndegeyo. Ndidali ndita phonyana ndi nthawi ya kukwerela kwa pafupi fupi ma mphindi makumi awiri. Ndidakhumudwa. Ndidayenera kudikilila ndege ina yopita ku Amsterdam!

    Simungathe kupanga ulendo wolumikiza kunka ku New York koma mutha kungo dikilila kunyamuka kotsatila, adandiwuza. Ndidazindikila kuchokera kunthawiyo, kuti ndidali wakuthekera kukwanitsa kukafika ku New York ndi kwa nthawi yochepa chabe kukayenda pa galimoto kunka ku Maryland. Choncho ndidayimbila ku New York ndi kuwawuza abusawo za nthawi imene ndikadati ndikafikile kumeneko ndi kutinso tikafunikila kuyendetsedwa mwachangu kunka ku Maryland. Ndidamutsimikizila kuti tidali mu nthawi yabwino ndi kuti pologalamu ikakhalako posalabadila kuchedwa kwa pang’ono.

    Ku Amsterdam, ndidakwera ndege yanga yakundilumikizitsa ku New York ndi chilimbikitso podziwa kuti adali akunyamuka posakhalitsa ndi kuti ndikhala ndili pa

    Enjoying the preview?
    Page 1 of 1